Exodus 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akakhala kuti anali yekha, adzachokanso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pobwerapo, mkazi wakeyo adzapita naye limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akalowa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akalowa ali yekha azituruka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wace azituruka naye.