Exodus 21:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ng'ombe ya munthu wina ikapha ng'ombe ya mnzake, anthu aŵiriwo agulitse ng'ombe yamoyoyo, ndipo ndalama zake agaŵane. Nyama yake ya ng'ombe yakufayo agaŵanenso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzace, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zace; naigawe, ndi yakufa yomweyo.