Exodus 21:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kukadziŵika kuti ng'ombeyo inkangogunda anthu, mwiniwake osaimanga, mwiniwakeyo ayenera kulipira pakupereka ng'ombe yamoyo chifukwa cha yakufayo. Tsono ng'ombe yakufayo ikhale yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena kudadziwika kuti ng'ombeyo ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yace.