Exodus 21:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mbuyake adampatsa mkazi, ndipo adamubalirapo ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo pamodzi ndi anawo onse ndi a mbuyakeyo. Tsono mwamuna yekhayo ndiye adzachoke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akampatsa mkazi mbuye wace, ndipo akambalira ana amuna ndi akazi, mkaziyo ndi ana ace azikhala a mbuye wace, ndipo azituruka ali yekha.