Exodus 21:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo mbuyakeyo abwere ndi kapoloyo ku Nyumba ya Mulungu. Abwere naye ku chitseko kapena ku mphuthu ya chitseko, ndipo amuboole khutu lake. Motero adzakhala kapolo wa mbuyakeyo moyo wake wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake amboole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mbuye wakeyo abwere naye kwa Yehova. Abwere naye pa chitseko kapena pa mphuthu zachitseko ndipo abowole khutu lake ndi chitsulo. Ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mbuye wace azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wace amboole khutu lace ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira nchito masiku onse.