Exodus 21:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mkaziyo amuipira m'maso mbuye amene ankafuna kumkwatirayo, amlole kuti aomboledwe. Sangathe konse kumgulitsa kwa anthu achilendo chifukwa chakuti sadamchite zokhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akapanda kumkonda mbuye wace, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu acilendo, popeza wacita naye monyenga.