Exodus 22:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati munthu wina anasungitsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa, kapena chiweto chilichonse ndipo chiweto chija nʼkufa kapena kupweteka kapena kutengedwa popanda wina kuona,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akaikiza buru, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena coweta cina kwa mnansi wace, ndipo cikafa, kapena ciphwetekwa, kapena wina acipitikitsa osaciona munthu;