Exodus 22:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiye kuti anthu awiriwo ayenera kulumbira pamaso pa Mulungu kuti asatenge chinthu cha mnzake. Zikatero mwini katundu uja avomereze zimenezi ndipo asabwezeredwe kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanaturutsa dzanja lace pa cuma ca mnansi wace; ndipo mwiniyo azibvomereza, ndipo asalipe.