Exodus 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu.