Exodus 22:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza copfunda cace ndi ici cokha, ndico cobvala ca pathupi pace; azipfundira ciani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandipfuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wacisomo.