Exodus 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Litamturukira dzuwa, pali camwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wace.