Exodus 22:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; cifukwa cace musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agaru.