Exodus 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akaikiza ndalama kapena cuma kwa mnansi wace, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe cowirikiza.