Exodus 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbalayo ikapanda kupezeka, mwini nyumba uja atengedwe ndi kufika naye pamaso pa Mulungu, kuti ziwoneke ngati katunduyo sadatenge ndi iyeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lace pa cuma ca mnansi wace.