Exodus 22:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mlandu uti wonse wa colakwa, kunena za ng'ombe, za buru, za nkhosa, za cobvala, za kanthu kali konse kotayika, munthu anenako kali kace; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe cowirikiza kwa mnansi wace.