Exodus 23:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma caka cacisanu ndi ciwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo ndipo zotsalira iwowa zoweta za kubusa zizidye; momwemo uzicita ndi munda wako wamphesa, ndimundawakowaazitona.