Exodus 23:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uzicita nchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lacisanu ndi ciwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi buru wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakaziwako ndi mlendo atsitsimuke.