Exodus 23:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka m'Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto. “Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda cotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unaturuka m'Aigupto; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;