Exodus 23:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda. “Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za nchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi madyerero a kututa, pakutha caka, pamene ututa nchito zako za m'munda.