Exodus 23:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti. “Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.