Exodus 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uzibweca nazo zoyambayamba za m'munda mwako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace. Mulungu aloniezana nao za Kanani.