Exodus 23:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kucita monga mwa nchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.