Exodus 23:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku Nyanja Yaikulu ya Afilisti, ndi kuyambiranso ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Ndidzakupatsani mphamvu zopambanira anthu a m'dzikolo, ndipo mudzaŵapirikitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisiti, ndi kuyambira kucipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.