Exodus 23:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usalandira cokometsera mlandu; pakuti cokometsera mlandu cidetsa maso a openya, nicisanduliza mlandu wa olungama,