Exodus 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi masveruzo onse; ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzacita.