Exodus 24:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m'maŵa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ya mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena. Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.