Exodus 24:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga buku la Cipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzacita, ndi kumvera.