Exodus 24:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adatenga magazi am'mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “Magazi ameneŵa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onseŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati Taonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mau awa onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Taonani mwazi wa cipangano, cimene Yehova anacita nanu, kunena za mau awa onse,