Exodus 25:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upange mbale ndi zipande zofunika popereka lubani, ndiponso mitsuko ndi mabeseni ofunika pa zopereka za chakumwa. Zonsezi zikhale za golide wabwino kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzipanga mbale zace, ndi zipande zace, ndi mitsuko yace, ndi zikho zace zakuthira nazo; uzipanga za golidi woona.