Exodus 25:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Upange choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zikhale zagolide, ndipo uchisule ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, zonsezo zipangidwire kumodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzipanga coikapo nyali ca golidi woona; coikapoco cisulidwe mapangidwe ace, tsinde lace ow thupi lace; zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zikhale zocokera m'mwemo;