Exodus 26:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Upange chihema chamapemphero ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Nsalu zimenezi uzipete bwino ndi zithunzi za akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzipanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzipanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, nchito ya mmisiri.