Exodus 26:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Upangenso magonga makumi asanu m'mbali mwake mwa nsalu yotsirizira ya chinsalu chimodzi, ndiponso magonga makumi asanu pa nsalu yotsiriza inayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo ya cilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo ya cilumikizano cina.