Exodus 26:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo upange masinde makumi anai asiliva pansi pa mafulemu makumi aŵiriwo. Pansi pa fulemu lililonse pakhale masinde aŵiri ogwirizira zolumikizira ziŵiri zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri;