Exodus 26:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafulemu ameneŵa apangodya azilumikizidwa kuyambira pansi mpaka pa chigwinjiri chapamwamba. Umu ndimo m'mene akhalire mafulemu aŵiri amene akupanga ngodya ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala angodya ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwace ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala a ngondya ziwiri.