Exodus 26:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Usoke nsalu yotchingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Ndipo nsaluyo uipete ndi zithunzi za akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uziomba nsaru yocinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi nchito ya mmisiri;