Exodus 26:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tebulo lija uliike kunja kwa nsalu yochingayo. Choikaponyale chija uchiike chakumwera kwake kwa chihemacho, mopenyana ndi tebulolo, limene likhale mbali yakumpoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nuziika gomelo kunja kwa nsaru yocinga, ndi coikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto,