Exodus 26:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa chipata choloŵera m'chihemamo, uikepo nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uziomba nsaru yotsekera pa khomo la bema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula.