Exodus 26:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muutali mwake nsalu iliyonse ikhale mamita 14, ndipo muufupi mwake pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsarukhumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.