Exodus 27:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Upange guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda: muutali mwake likhale masentimita 229, muufupi mwake chimodzimodzi: masentimita 229, msinkhu wake masentimita 137.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wasitimu, utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, guwa la nsembelo likhale lampwamphwa, ndi msinkhu wace mikono itatu.