Exodus 27:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nsanamira zake 20 ndi masinde ake 20 zikhale zamkuŵa, koma ngoŵe za nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zikhale zasiliva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zikhale zasiliva.