Exodus 27:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto m'utali mwake pakhale nsalu zochingira za mikono zana limodzi m'utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemonso pa mbali ya kumpoto m'utali mwace pakhale nsaru zocingira za mikono zana limodzi m'utali mwace; ndi nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsicizo ndi mitanda yace zikhale zasiliva.