Exodus 27:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzimodzi pa mbali ina pakhalenso nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zochingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ku mbali inayo kukhale nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pa mbali yina pakhale nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu.