Exodus 27:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anai. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotchinga yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira ndiponso yofewa yosalala. Nsaluyo ikhale yotalika mamita asanu ndi anayi, yopangidwa ndi anthu aluso. Pakhalenso mizati yake inayi ndi matsinde akenso anayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.