Exodus 27:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutalika kwake kwa bwalolo kukhale mamita 46, muufupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu zochingazo zikhale za thonje losankhidwa bwino kwambiri ndi lopikidwa, ndipo masinde ake akhale amkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.