Exodus 27:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aroni ndi ana ake aamuna aziyatsa nyale m'chihema chamsonkhanomo amakumana ndi anthu ake, kunja kwa chochinga, patsogolo pa miyala yaumboni ija. Tsono nyalezo ziziyaka kumeneko kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Lamulo limeneli adzalisunge Aisraele ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchihema cha msonkhano, koma kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, Aaroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pakati pa Aisraeli pa mibado yonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.