Exodus 27:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pambuyo pake upange bwalo la chihema, lochingidwa. Chakumwera kwake kukhale nsalu zochinga za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, kutalika kwa mbali imodzi kukhale mamita 46.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zochingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Upangenso bwalo la cihema; pa mbali yace ya kumwela, kumwela, pakhale nsaru zocingira zakubwaloza nsaru ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wace wa pa mbali imodzi mikono zana;