Exodus 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake amuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ace amuna pamodzi naye, mwa ana a Israyeli, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara, ana a Aroni.