Exodus 28:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maina aowo uŵalembe mozokota pa miyala iŵiriyo, potsata luso la mmisiri wozokota miyala. Ndipo miyalayo uiike m'zoikamo zake zagolide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi,