Exodus 28:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uike miyala iŵiri imeneyi pa tizikwewo tam'mapewa ta efodi, ngati chikumbutso cha ana a Israele. Mwa njira imeneyi, Aroniyo azidzanyamula pa mapewa mainawo, ndipo Chauta azidzaŵakumbukira iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ulike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso ca ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ace awiri, akhale cikumbutso pamaso pa Yehova.