Exodus 28:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono usoke chovala chapachifuwa, chopetedwa mwaluso, chomavala poweruza. Mapangidwe ake akhale ngati a efodi, ndiye kuti a nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Upange chovala chapachifuwa chogwiritsa ntchito poweruza mlandu ndipo uchipange mwaluso kwambiri. Uchipange ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Upangenso capacifuwa ca ciweruzo, nchito ya mmisiri; uciombe mwa ciombedwe ca efodi; uciombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.